Mawu a M'munsi
b Akatswiri ena amanena kuti mawu achiheberi okuluwika, amene anawamasulira kuti “ndileke” pa Eksodo 32:10 ndi opempha Mose kuti akhale mkhalapakati kapena kuti aime pakati pa Yehova ndi mtundu wa Isiraeli. (Sal. 106:23; Ezek. 22:30) N’zoonekeratu kuti Mose anali womasuka kufotokoza maganizo ake kwa Yehova.