Mawu a M'munsi
a Ulosi unaneneratu kuti zinthu zina zimene zinkachitika pa misonkhano yachikhristu m’nthawi ya atumwi zidzatha. Mwachitsanzo, panopa ‘sitilankhula malilime’ kapena “kunenera.” (1 Akor. 13:8; 14:5) Ngakhale zili choncho, malangizo a Paulo akutithandiza kumvetsa mmene tiyenera kuchitira misonkhano yachikhristu masiku ano.