Mawu a M'munsi
a Ngakhale kuti m’Baibulo simupezeka mawu akuti “makolo amene akulera okha ana” kapena “makolo amene sali pa banja,” mawu akuti “mayi wamasiye” ndi “mwana wamasiye” amapezekamo kambirimbiri. Zimenezi zikusonyeza kuti nthawi imene Baibulo linkalembedwa panali makolo ena amene anali kulera okha ana.—Yesaya 1:17.