Mawu a M'munsi
c Mulungu ndi amene anabweretsa Chigumula chimenechi ndipo zikuoneka kuti chinafafaniziratu munda wa Edeni. Lemba la Ezekieli 31:18 limasonyeza kuti pofika zaka za m’ma 1600 B.C.E. “mitengo ya mu Edeni” inali itatha kale. Choncho onse amene anayesetsa kufunafuna malo amene panali munda wa Edeni anangotaya nthawi chifukwa sakanaupeza.