Mawu a M'munsi
b Lemba la Levitiko 19:18 limanena kuti: “Usabwezere choipa kapena kusungira chakukhosi anthu amtundu wako. Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” Atsogoleri a chipembedzo chachiyuda ankanena kuti mawu akuti “anthu amtundu wako” ndiponso “mnzako” amanena za Ayuda okha. Chilamulo chinkauza Aisiraeli kuti azikhala osiyana ndi anthu a mitundu ina. Komabe, sichinkalimbikitsa maganizo amene atsogoleri achipembedzo ankalimbikitsa m’nthawi ya atumwi. Atsogoleriwo ankati munthu aliyense wa mtundu wina anali mdani wawo ndipo sanali woyenera kumukonda.