Mawu a M'munsi
b “Mawu achifatse apansipansi” amenewa ayenera kuti anali a mngelo amene anagwiritsidwanso ntchito kunena “mawu a Yehova” amene ali palemba la 1 Mafumu 19:9. Pa vesi 15 anangomutchula kuti “Yehova.” Zimenezi zingatikumbutse mngelo yemwe Yehova anamugwiritsira ntchito kutsogolera Aisiraeli m’chipululu. Ponena za mngelo ameneyu, Mulungu anati: “Dzina langa lili mwa iye.” (Ekisodo 23:21) Ngakhale kuti Baibulo silinena mwatchutchutchu kuti mngelo amene analankhula ndi Eliya anali Yesu, mfundo yofunika kuidziwa ndi yakuti Yesu asanakhale munthu Yehova ankamugwiritsa ntchito monga “Mawu,” kapena kuti Womulankhulira.—Yohane 1:1.