Mawu a M'munsi
a Nkhani imene Yesu ndi Petulo ankakambirana inali yokhudza Khristu komanso udindo wake osati yokhudza za udindo umene Petulo adzakhale nawo. (Mateyu 16:13-17) Patapita nthawi, Petulo ananena kuti Yesu ndiye thanthwe limene mpingo unamangidwapo. (1 Petulo 2:4-8) Nayenso mtumwi Paulo anatsimikizira kuti Yesu, osati Petulo, ndi amene ali ‘mwala wapakona wa maziko’ a mpingo wachikhristu.—Aefeso 2:20.