Mawu a M'munsi
b Yesu komanso atumwi ake anachenjeza kuti mu mpingo wachikhristu mudzakhala anthu amene azidzaphunzitsa zinthu zampatuko. (Mateyu 13:24-30, 36-43; 2 Timoteyo 4:3; 2 Petulo 2:1; 1 Yohane 2:18) Mawu amenewa anakwaniritsidwa pamene m’zaka za ma 100 C.E. anthu ena mu mpingo wachikhristu anayamba kutengera miyambo yachikunja komanso kusakaniza ziphunzitso za m’Baibulo ndi mfundo zimene Agiriki ankaphunzitsa.