Mawu a M'munsi
a Zimbalangondo zoderapo za ku Siriya, zimene zinkapezeka ku Palesitina, zinkakhala zikuluzikulu zolemera pafupifupi makilogalamu 140. Zimbalangondo zimenezi zinkatha kupha munthu kapena nyama ndi mapazi awo akuluakulu. M’dera limeneli munkapezekanso mikango yambiri. Lemba la Yesaya 31:4 limanena kuti ngakhale “abusa ambirimbiri” sakanatha kuthamangitsa “mkango wamphamvu” kuti usiye nyama imene wagwira.