Mawu a M'munsi
a Ayuda akale ankaona kuti zimenezi zinali zochititsa manyazi kwambiri. Buku lachiwiri la Amakabeo lomwe anawonjezera m’Mabaibulo ena, limanena kuti Ayuda ambiri anakwiya pamene mkulu wa ansembe dzina lake Jason ankafuna kuti ku Yerusalemu kukhale malo ochitira masewera ngati omwe anali ku Girisi.—2 Amakabeo 4:7-17.