Mawu a M'munsi
e Mapale a nkhani zachuma amene alipo amanena za zaka zonse za ulamuliro wa mafumu amene amati analamulira mu Ufumu Wachiwiri wa Babulo. Tikaphatikiza zaka zonse zimene mafumuwa analamulira, n’kuwerengetsera chobwerera m’mbuyo kuyambira pa Nabonidus, mfumu yomaliza mu ufumuwu, zimasonyeza kuti Yerusalemu anawonongedwa m’chaka cha 587 B.C.E. Komabe, kawerengedwe kameneka kangakhale kolondola pokhapokha ngati mfumu iliyonse yatsopano inkayamba kulamulira nthawi yomweyo mfumu ina ikangosiya kulamulira.