Mawu a M'munsi
a Nthano ina yachigiriki imati mumzinda wa Gordium, womwe unali likulu la dera la Fulugiya, munali galeta lomwe linamangiriridwa kumtengo ndi mfundo yovuta kwambiri kumasula. Mwini wa galetalo anali munthu wina yemwe anayambitsa kumanga mzindawo dzina lake Gordius. Yemwe akanatha kumasula mfundoyo ndi munthu yekhayo amene akanagonjetsa chigawo cha Asia.