Mawu a M'munsi
b N’zochititsa chidwi kuti Zamora anagwiritsa ntchito dzina la Mulungu, osati dzina laudindo chabe, m’kalata yake yodandaula yopita kwa papa ku Rome. M’kalata ya Zamora yomwe inamasuliridwa m’Chisipanishi, dzina la Mulungu limeneli linalembedwa kuti “Yahweh.” Sizikudziwika kuti dzinali linalembedwa bwanji m’kalata yake yoyambirira ya m’Chilatini imene inatumizidwa kwa papa. Koma ponena za mabuku amene Zamora anamasulira ndiponso mmene anagwiritsira ntchito dzina la Mulungu, onani bokosi lakuti “Kumasulira Dzina la Mulungu,” patsamba 19.