Mawu a M'munsi
a Mu nkhani yoyamba, tinaona kuti Esitere yemwe anali mwana wamasiye, analeredwa ndi Moredekai yemwe anali mwana wa m’bale wa bambo ake. Koma Moredekai anali wamkulu kwambiri poyerekeza ndi Esitere. Kenako Esitere anasankhidwa kuti akhale mkazi wa Ahasiwero mfumu ya ku Perisiya. Hamani, yemwe anali mlangizi wa mfumu, anakonza chiwembu choti aphe Moredekai limodzi ndi Ayuda onse. Moredekai anauza Esitere kuti apite kwa mfumu kukapempha kuti Ayuda asaphedwe.—Onani nkhani yakuti “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo—Analimba Mtima Kuteteza Anthu a Mulungu,” mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 2011.