Mawu a M'munsi
b Mfumu inalola kuti Ayuda amenyenso nkhondo tsiku lotsatira n’cholinga chakuti amalize kugonjetsa adani awo. (Esitere 9:12-14) Mpaka pano, chaka chilichonse Ayuda amakumbukirabe kupambana kumeneku pa chikondwerero chotchedwa Purimu. Mwambowu anaupatsa dzina limeneli potengera dzina la maere amene Hamani anachita aja.