Mawu a M'munsi
a Mfundo yoti Yehova ndi Atate imatchulidwa kawirikawiri m’Baibulo. Mwachitsanzo, Yesu anagwiritsa ntchito mawu akuti “Atate” kokwanira ka 65 m’Mauthenga Abwino a Mateyu, Maliko ndi Luka komanso ka 100 mu Uthenga Wabwino wa Yohane. Nayenso Paulo anatchula Mulungu kuti “Atate” maulendo 40 m’makalata ake. Yehova ndi Atate wathu chifukwa ndi amene anatipatsa moyo.