Mawu a M'munsi
c Lemba la Danieli 2:44 limanena za “kuthetsa maufumu ena onsewo.” Apa akunena za maufumu omwe akuimiridwa ndi mbali zosiyanasiyana za chifanizirochi. Koma ulosi wina m’Baibulo umanena kuti “mafumu a dziko lonse lapansi” adzasonkhanitsidwa kuti alimbane ndi Yehova pa “tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” (Chiv. 16:14; 19:19-21) Choncho maufumu a m’chifanizirocho komanso maufumu onse a padziko lapansi adzawonongedwa pa Aramagedo.