Mawu a M'munsi
a Nanga bwanji ngati kamwanako m’mimba mwa mayiyo kakuoneka kuti sikadzabadwa kabwinobwino, kapenanso ngati zikuoneka kuti adzabereka ana angapo? Zikatero, ena amasankha kuchotsa mimbayo. Amayi amene amatsatira njira yochotsa mazira m’mimba n’kukawaphatikiza ndi umuna, nthawi zambiri amabereka ana awiri, atatu kapena kuposerapo. Zimenezi zimabweretsa mavuto monga kubereka ana masiku asanakwane ndiponso kutaya magazi ambiri pobereka. Chotero mayi amene akuoneka kuti adzabereka ana ambiri amamulimbikitsa kuti asankhe ana oti abereke ndipo enawo awaphe. Kuchita zimenezi n’kuchotsa mimba kwadala ndipo n’chimodzimodzi ndi kupha munthu.—Eks. 21:22, 23; Sal. 139:16.