Mawu a M'munsi
a Palembali mawu akuti “pamene dziko linakhazikika” amanena za kuberekana kwa anthu, choncho lembali likunena za ana a anthu oyambirira. Nanga n’chifukwa chiyani Yesu ananena za Abele, kuti anakhalapo “pamene dziko linakhazikika” pomwe woyamba kubadwa anali Kaini? N’chifukwa choti zochita za Kaini zinasonyeza kuti anali wopandukira Yehova Mulungu. Mofanana ndi makolo ake, zikuoneka kuti Kaini sali m’gulu la anthu odzaukitsidwa komanso kuwomboledwa ku uchimo ndi imfa.