Mawu a M'munsi
a Fanizo la Yesuli linali logwirizana ndi zimene zinkachitika pa nthawiyo. Ayuda ankaona kuti kuchereza alendo kunali kofunika kwambiri. Banja linkangophika chakudya chokwana tsiku limodzi, choncho nthawi zambiri sankakhala ndi chakudya chotsala. Komanso ngati ali osauka, banja lonse linkagona pansi m’chipinda chimodzi.