Mawu a M'munsi
b Akatswiri ofukula zinthu zakale apeza nsanja zazitali zokhala ndi masitepe ku Sinara. Baibulo limanena kuti anthu amene ankamanga nsanja ya Babele ankamangira njerwa, osati miyala, ndipo ankagwiritsa ntchito phula mmalo mwa matope. (Genesis 11:3, 4) Buku la The New Encyclopædia Britannica linanena kuti ku Mesopotamiya miyala inali “yosowa kwambiri, mwinanso sinkapezeka n’komwe,” pamene phula linkapezeka lambiri.