Mawu a M'munsi
b Tsiku la Nisani 15 linali tsiku loyamba la Chikondwerero cha Mikate Yopanda Chofufumitsa ndipo nthawi zonse linkakhala tsiku la sabata. Koma m’chaka cha 33 C.E. tsikuli linali pa Loweruka, lomwe mlungu uliwonse linkakhala la sabata. Choncho popeza kuti tsiku la Nisani 15 mu 33 C.E. linali la sabata pa zifukwa ziwiri zimenezi, ankanena kuti linali Sabata “lalikulu.”—Werengani Yohane 19:31, 42.