Mawu a M'munsi
a Yehova anali atachititsa kuti m’dzikoli mugwe chilala kwa zaka zitatu ndi hafu, n’cholinga choti anthu adziwe kuti Baala anali mulungu wopanda mphamvu. Anthu amene ankalambira Baala ankakhulupirira kuti ndi mulungu wogwetsa mvula komanso wothandiza kuti nthaka ikhale ndi chonde. (1 Mafumu chaputala 18) Onani nkhani zakuti, “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo” mu Nsanja ya Olonda ya January 1 ndi April 1, 2008.