Mawu a M'munsi
a Akatswiri ena amati azichimwene ake a Yosefe anaona kuti bambo awo anapatsa Yosefe mkanjo chifukwa ankafuna kuti Yosefeyo adzatenge madalitso amene ankaperekedwa kwa mwana woyamba kubadwa. Ankadziwanso kuti Yosefe anali mwana woyamba wa Rakele, mkazi amene Yakobo ankamukonda kwambiri. Komanso Rubeni, mwana woyamba wa Yakobo, anali atagona ndi Biliha, mkazi wamng’ono wa bambo ake. Uku kunali kunyoza bambo akewo komanso kupeputsa udindo wake monga mwana woyamba.—Genesis 35:22; 49:3, 4.