Mawu a M'munsi
b Anthu akale a ku Iguputo ankakonda kwambiri mikate komanso makeke. Ankaphika mikate komanso makeke a mitundu yosiyanasiyana yoposa 90. Choncho mkulu wa ophika mikateyu anali munthu wotchuka kwambiri. Komanso mkulu wa operekera chikhoyu ankayang’anira anthu ogwira ntchito panyumba ya mfumu. Anthuwa ankaonetsetsa kuti vinyo kapena mowa umene unkaperekedwa kwa Farao unali wabwino kwambiri. Ankaonetsetsanso kuti zinthuzi sizinathiridwe poizoni ndi anthu ofuna kupha mfumu, chifukwa ziwembu zoterezo zinkachitikachitika. Nthawi zambiri mkulu wa operekera chikho ankakhalanso mlangizi wa mfumu.