Mawu a M'munsi
d M’Mawu a Mulungu muli nkhani zina “zovuta kuzimvetsa” ndipo zina zimapezeka m’makalata a Paulo. Koma anthu onse amene analemba Baibulo ankatsogoleredwa ndi mzimu woyera. Mzimu womwewo umathandiza Akhristu masiku ano kumvetsa mfundo za m’Malemba. Timatha kumvetsa ngakhale zitakhala “zinthu zozama za Mulungu.”—2 Pet. 3:16, 17; 1 Akor. 2:10.