Mawu a M'munsi
a Buku lina linanena kuti “pogwiritsa ntchito njirayi, akatswiri amatha kudziwa nthawi imene zinthu zinalembedwa. Amayerekezera kalembedwe ka chinthu chimene akufuna kufufuzacho, ndi kalembedwe ka zinthu zina zakale.” (Manuscripts of the Greek Bible) Pa nthawi inayake anthu amakhala ndi kalembedwe kofanana, koma pakapita nthawi zimasintha ndipo amayamba kalembedwe kena. Choncho akatswiriwa amatha kuzindikira nthawi yomwe chinthu chinalembedwa poona kalembedwe kake.