Mawu a M'munsi
b Dzina la Baibuloli limatanthauza 70 ndipo ena amaganiza kuti linamasuliridwa ndi anthu 72. Zikuoneka kuti Baibuloli linayamba kumasuliridwa ku Iguputo pafupifupi zaka 300 Yesu asanabadwe ndipo n’kutheka kuti linamalizidwa patapita zaka 150. Baibulo limeneli ndi lofunikabe masiku ano chifukwa limathandiza akatswiri a Baibulo kumvetsa tanthauzo la mawu kapena mavesi ena a m’Malemba Achiheberi.