Mawu a M'munsi
b Lemba la Ezekieli 37:1-14 komanso la Chivumbulutso 11:7-12, limanena za kumasulidwa kwa anthu a Mulungu mu ukapolo komwe kunachitika mu 1919. Komabe ulosi wa pa Ezekieliwu ukunena za kumasulidwa kwa anthu onse a Mulungu amene anakhala mu ukapolo kwa nthawi yaitali. Pamene ulosi wa pa Chivumbulutso ukunena za kuyambiranso kwa kagulu ka abale odzozedwa komwe kanasankhidwa mu 1919 ndipo kakhala kakutsogolera anthu a Mulungu.