Mawu a M'munsi
b Tingati Sara anali mchemwali wake wa Abulahamu. Onsewa bambo awo anali Tera koma amayi awo anali osiyana. (Genesis 20:12) Masiku ano n’zosayenera munthu kukwatira mchemwali wake. Koma tikumbukire kuti pa nthawiyo zinthu zinali zosiyana ndi pano. Nthawi imeneyo panali pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene Adamu ndi Hava anakhala opanda ungwiro. Choncho munthu akakwatirana ndi m’bale wake wapafupi, sizinkabweretsa mavuto alionse kwa ana obadwawo. Koma patatha zaka 400, moyo unayamba kukhala waufupi ngati masiku ano. Choncho m’Chilamulo cha Mose munali lamulo loletsa munthu kukwatirana ndi wachibale wapafupi.—Levitiko 18:6.