Mawu a M'munsi
b Zikuoneka kuti panali akatswiri ena m’mbuyomo amene anamasulirapo Baibulo la Chipangano Chatsopano m’Chiheberi. Mmodzi wa anthu amenewa anali Simon Atoumanos ndipo analimasulira cha m’ma 1360. Wina anali Oswald Schreckenfuchs, wa ku Germany ndipo anamasulira Baibulo lake cha m’ma 1565. Mabaibulo amenewa sanasindikizidwe ndipo sapezeka masiku ano.