Mawu a M'munsi
a Mzinda wa Arimateya uyenera kuti ndi umene umadziwikanso kuti Rama, womwe masiku ano amauti Rentis (Rantis). Kumeneku ndi kumene kunali kwawo kwa mneneri Samueli, ndipo mzindawu unali pa mtunda wa makilomita pafupifupi 35 kumpoto chakumadzulo kwa Yerusalemu.—1 Sam. 1:19, 20.