Mawu a M'munsi
a Azimayi ena omwe amadwala matenda osokonezeka maganizo akangobereka, (Postpartum Depression) amalephera kukonda ana awo. Komabe azimayi amenewa sayenera kudziimba mlandu chifukwa cha zimenezi. Bungwe lina linanena kuti, matendawa “amayamba chifukwa cha kusokonekera kwa zinthu zina m’thupi . . . osati chifukwa cha zinthu zimene mayiyo wachita kapena walephera kuchita.” (U.S. National Institute of Mental Health) Kuti mumve zambiri zokhudza matendawa, werengani nkhani yakuti “Understanding Postpartum Depression,” mu Galamukani! yachingelezi ya June 8, 2003.