Mawu a M'munsi
b TANTHAUZO LA MAWU ENA: Kugwirira mwana kumatanthauza zinthu zimene munthu wamkulu angachite kwa mwana n’cholinga choti akhutiritse chilakolako chake cha kugonana. Apa tikutanthauza zinthu monga kugona mwanayo kwenikweni, kumugona mkamwa kapena kumatako, kumuseweretsa maliseche, mabere kapena matako. Tizikumbukira kuti mwana akagwiriridwa amakhala kuti wachitiridwa nkhanza kwambiri ndipo iyeyo ndi wosalakwa. N’zoona kuti amene amagwiriridwa kawirikawiri ndi atsikana koma anyamata ambiri amagwiriridwanso. Nthawi zambiri amuna ndi amene amagwirira ana koma akazi ena amachitanso zimenezi.