Mawu a M'munsi
a Kodi mumaona kuti simukuchita zambiri potumikira Yehova? Kodi mumakayikira zoti Mulungu angakugwiritseni ntchito? Kapena kodi mumaona kuti simukufunika kulola kuti Yehova azikugwiritsani ntchito mmene akufunira? Munkhaniyi tiona njira zimene Yehova angatithandizire kuti tikhale ndi mtima wofuna kuchita zinthu zogwirizana ndi cholinga chake komanso mphamvu zochitira zinthuzo.