Mawu a M'munsi
a Kuyambira pa Pentekosite mu 33 C.E., Yehova wakhala akupatsa Akhristu ena chiyembekezo chapadera chokalamulira ndi Mwana wake kumwamba. Koma kodi Akhristu amenewa amadziwa bwanji kuti apatsidwa mwayi woti adzapite kumwamba? Nanga chimachitika n’chiyani munthu akapatsidwa mwayi wapaderawu? Nkhaniyi iyankha mafunso amenewa ndipo mfundo zake zikugwirizana ndi zamunkhani imene inatuluka mu Nsanja ya Olonda ya January 2016.