Mawu a M'munsi
a Atumiki a Yehova ambiri masiku ano akuvutika ndi ukalamba kapena matenda aakulu. Ndipo tonsefe timatopa nthawi zina. Choncho tikhoza kuona kuti sitingakwanitse kuthamanga pa mpikisano. Munkhaniyi tikambirana zimene tingachite kuti tithamange mopirira mpikisano umene mtumwi Paulo anatchula, n’cholinga choti tidzapeze mphoto ya moyo wosatha.