Mawu a M'munsi
a Yehova ndi Atate wachikondi, wanzeru komanso woleza mtima. Makhalidwewa amaonekera bwino tikaganizira mmene analengera zinthu zonse komanso cholinga chake chodzaukitsa anthu amene anamwalira. Munkhaniyi, tikambirana mafunso ena omwe tingakhale nawo okhudza kuukitsidwa kwa akufa ndipo tiona mmene tingasonyezere kuyamikira Yehova chifukwa cha chikondi, nzeru komanso kuleza mtima kwake.