Mawu a M'munsi
a Yesu anauza asodzi odzichepetsa komanso akhama kuti akhale ophunzira ake. Masiku anonso, Yesu akuitana anthu a makhalidwe ngati amenewa kuti akhale asodzi a anthu. Munkhaniyi tikambirana zimene ophunzira Baibulo angachite ngati akukayikira kuti sangakwanitse kukhala ophunzira a Yesu n’kumagwira nawo ntchito yolalikira uthenga wabwino.