Mawu a M'munsi
a Yosefe, Naomi, Rute, Mlevi wina komanso mtumwi Petulo anakumana ndi zinthu zimene zinachititsa kuti mitima yawo isweke. Munkhaniyi, tiona mmene Yehova anawalimbikitsira komanso kuwapatsa mphamvu. Tionanso zimene tikuphunzira kuchokera kwa anthu amenewa komanso mmene Yehova anawathandizira mwachikondi.