Mawu a M'munsi
a Tsiku la 27 March 2021, lidzakhala lapadera kwambiri kwa Mboni za Yehova. Madzulo a tsiku limeneli tidzachita mwambo wokumbukira imfa ya Khristu. Anthu ambiri amene adzapezeke pamwambowu ndi amene Yesu anawatchula kuti a “nkhosa zina.” Kodi mu 1935, a Mboni za Yehova anadziwa mfundo yachoonadi iti? Kodi a nkhosa zina akuyembekezera kudzasangalala ndi zinthu ziti pambuyo pa chisautso chachikulu? Nanga amatamanda bwanji Mulungu ndi Khristu akapezeka pamwambo wa Chikumbutso?