Mawu a M'munsi
a Mtumwi Yohane ayenera kuti ndi “wophunzira amene Yesu anali kumukonda kwambiri.” (Yoh. 21:7) Choncho ngakhale kuti iye anali wachinyamata, ayenera kuti anali ndi makhalidwe ambiri abwino. Patapita nthawi, ali wachikulire, Yehova anamugwiritsa ntchito kulemba zambiri zokhudza chikondi. Munkhaniyi, tikambirana zina zimene iye analemba komanso zomwe tingaphunzire pa chitsanzo chake.