Mawu a M'munsi
a Popeza si ife angwiro, nthawi zina tingalankhule kapena kuchita zinthu zimene zingakhumudwitse abale ndi alongo athu. Ndiye zikatere tiyenera kuchita chiyani? Kodi timayesetsa kuti tikhalenso pamtendere ndi abale athuwo? Nanga kodi timapepesa mofulumira? Kapena kodi timaona kuti ngati akhumudwa ndi vuto lawo osati lathu? Kapenanso bwanji ngati sitichedwa kukhumudwa ndi zimene alankhula kapena kuchita? Kodi timadzikhululukira n’kumanena kuti ndi mmene ndilili basi? Kapena kodi timaona kuti limeneli ndi vuto lathu ndipo tiyenera kusintha?