Mawu a M'munsi
a Kuti zinthu ziziyenda bwino m’banja, aliyense afunika kudziwa zimene ayenera kuchita komanso kumagwirizana ndi onse m’banjamo. Mwamuna ayenera kumatsogolera mwachikondi banja lake, mkazi wake amafunika kumuthandiza ndipo ana ayeneranso kumamvera makolo awo n’kumachita zinthu mogwirizana nawo. Zimenezi ndi zimene zimachitikanso m’banja la Yehova. Mulungu ali ndi cholinga chabwino chokhudza anthufe ndipo tikamachita zinthu mogwirizana ndi cholinga chimenecho, tidzakhala m’banja la Yehova la anthu amene amamulambira mpaka kalekale.