Mawu a M'munsi
a Kodi munayamba mwamvapo Mkhristu amene watumikira Yehova kwa nthawi yayitali akunena kuti, ‘Sindinkayembekezera kuti dziko loipali likhala lilipobe mpaka pano.’ Tonsefe timafunitsitsa Yehova atawononga dziko loipali makamaka munthawi yovutayi. Komabe tiyenera kuphunzira kukhala oleza mtima. Munkhaniyi tikambirana mfundo za m’Baibulo zimene zingatithandize kuyembekezera nthawi imene Yehova adzachitepo kanthu. Tikambirananso mbali ziwiri zimene tiyenera kuyembekezera Yehova moleza mtima komanso madalitso amene anthu omwe amamuyembekezera adzapeze.