Mawu a M'munsi
b MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo wakhala akupemphera kwa Yehova nthawi zonse kuyambira ali wamng’ono. Ali mwana makolo ake anamuphunzitsa kupemphera. Ali mtsikana anayamba upainiya ndipo nthawi ndi nthawi ankapempha Yehova kuti adalitse utumiki wake. Patapita zaka mwamuna wake atayamba kudwala kwambiri, iye ankapempha Yehova kuti amuthandize kupirira mayesero amenewo. Panopa ndi wamasiye ndipo amapemphera nthawi zonse n’kumakhulupirira kuti Atate wake wakumwamba ayankha mapemphero ake monga mmene wakhala akuchitira m’mbuyo monsemu.