Mawu a M'munsi
a Timakonda kwambiri Yehova ndipo timafuna kuti tizimusangalatsa. Iye ndi woyera ndipo amayembekezera kuti anthu amene amamulambira akhalenso oyera. Kodi zimenezi ndi zothekadi kwa anthu ochimwafe? Inde n’zotheka. Kuphunzira mosamala malangizo amene mtumwi Petulo anapereka kwa Akhristu anzake komanso malangizo amene Yehova anapereka kwa Aisiraeli, kungatithandize kudziwa zimene tingachite kuti tikhale oyera m’makhalidwe athu onse.