Mawu a M'munsi
a Kuti tifike pobatizidwa, timafunika kusintha makhalidwe athu. Nkhaniyi itithandiza kudziwa kuti ndi makhalidwe ati amene amapanga umunthu wakale, chifukwa chake tiyenera kuwasiya komanso mmene tingachitire zimenezo. Nkhani yotsatira idzafotokoza zimene tingachite kuti tipitirize kuvala umunthu watsopano ngakhale pamene tabatizidwa.