Mawu a M'munsi
a Timayamikira kwambiri akulu achikondi chifukwa cha khama lomwe amasonyeza potisamalira. Munkhaniyi tikambirana mavuto 4 omwe akulu amakumana nawo nthawi zambiri. Tionanso mmene chitsanzo cha Paulo chingawathandizire masiku ano polimbana ndi mavuto amenewa. Nkhaniyi itithandiza kuti tiziwamvetsa ndiponso itilimbikitsa kuti tiziwasonyeza chikondi komanso kuwathandiza kuti azigwira ntchito yawo mosavuta.