Mawu a M'munsi
a Timoteyo anali mlaliki waluso wa uthenga wabwino. Komabe Paulo anamulimbikitsa kuti apitirizebe kupita patsogolo mwauzimu. Kumvera malangizowa, kukanachititsa kuti Yehova azimugwiritsa ntchito ndiponso azithandiza kwambiri abale ndi alongo ake. Kodi inunso mofanana ndi Timoteyo mukufunitsitsa kuti muzichita zambiri potumikira Yehova komanso Akhristu anzanu? Mosakayikira. Ndiye kodi ndi zolinga ziti zimene zingakuthandizeni? Nanga mungatani kuti mukhale nazo n’kumazikwaniritsa?